21/10/2024
LANGIZO LANGA LA ULERE KWA INU A MCP
Kuchoka mu 2020 kufika lero 2024 pamene MCP ikulamula boma
Zinthu zambiri zaonongeka ndipo palibe chimene chikuyenda bwino mdziko lino.
Tibwelere mmbuyo pang'ono chipani cha MCP chinalonjeza anthu kuti Feteleza azizagula motchipa pamtengo wa k4500 osati zamakuponi . Mnthawi imeneyo feteleza ankagulitsidwa pamtengo wa k18,000 ndipo ogula kwambiri unali pa k22,000 pamene wamakuponi umagulitsidwa pamtengo wa k4500.
Anthu analonjezedwa kuti madzi komanso magetsi azizaitanitsa ulere
Nthawi imeneyo cement ankagulitsidwa pamtengo wa k5000. Pamene sugar unali pa k600 nthawi imeneyo Sopo tinkagula wochapira k50 mafuta agalimoto anali pa k630.
MCP inaonetsa kuti ichita zinthu mmalawi muno ndipo amalawi onse anaika chikhulupiliro pa MCP.
Koma MCP zimene yaapanga amalawi pa zaka 4 izi amalawi atayiratu chiyembekezo ndi MCP ndipo sakufunanso kumva dzina la MCP.
MCP yaapanga amalawi kukhala anthu ozunzika kwambiri, yaawonetsa zibalo mudziko lawo lomwe akumva kuwawa palibe chikuyenda. Ndipo pano amalawi akuyenda olutsa lutsa chifukwa ambiri ma business awo anagwa, ena ntchito anachotsedwa, ena ananamizidwa kuti azawalemba ntchito anthu 1 million zomwe sizinatheke.
Ili ndi boma la bodza , lakatangale komanso la nkhanza chimene limadziwa boma ili ndi chipani cha MCP ndikumanga anthu basi.
Inu amene mkuimira chipani cha MCP 2025 musamale kwambiri chifukwa tikayang'ana pa ground apa kuchipani cha MCP sizilibwino. Anthu sakuyifuna or dontho msapusitsidwe ndimisonkho akumapanga a MCP anthu aja akumachita kuwagula aliyense akumapatsidwa t-shirt ndi k2000 kumanja kuti abwere kumsonkhano wawo.
Pangani chisankho chabwino nthawi isanathe kuli bwino muime panokha ngati simukuzifuna zipani zinazi. MCP amalawi sakuyifuna or pang'ono ndipo yaapangitsa amalawi ambiri kuzipha chifukwa cha mavuto osiyana siyana amene chapanga mdziko lino. MCP yaapanga amalawi kukhala osaukisitsa kwambiri. 2025 anthu sazaivotera MCP olira achuluka, amene akuimira pa tiketi ya MCP asamale kwambiri ndipo aganize kawiri katatu anthu ndiokwiya mmamidzi umu. Voti ya chaka cha mawa ndiya chikuwawe.
Malangizo anga awulere awa zili kwainu kugwilitsa ntchito nthawi isanathe.